1. Ndidzakukwezani, Yehova; pakuti mwandinyamutsa,Ndipo simunandikondwetsera adani anga,
2. Yehova, Mulungu wanga,Ndinapfuulira kwa Inu, ndipo munandiciritsa.
3. Yehova munabweza moyo wanga kumanda:Munandisunga ndi moyo, kuti ndingatsikire kudzenje.
4. Yimbirani Yehova, inu okondedwa ace,Ndipo yamikani pokumbukila ciyero cace.
5. Pakuti mkwiyo wace ukhala kanthawi kokha;Koma kuyanja kwace moyo wonse:Kulira kucezera,Koma mamawa kuli kupfuula kukondwera.
6. Ndipo ine, ndinanena m'phindu langa,Sindidzagwedezeka nthawi zonse.
7. Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu:Munabisa nkhope yanu; ndinaopa.
8. Ndinapfuulira kwa Inu, Yehova;Kwa Yehova ndinapemba:
9. M'mwazi mwanga muli phindu lanji, potsikira ine kudzenje?Ngati pfumbi lidzayamika Inu? ngati lidzalalikira coonadi canu?
10. Mverani, Yehova, ndipo ndicitireni cifundo:Yehova, mundithandize ndi Inu.
11. Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera;Munandibvula ciguduli canga, ndipo munandibveka cikondwero:
12. Kuti ulemu wanga uyimbire Inu, wosakhala cete.Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.
Werengani mutu wathunthu Masalmo 30