1. Yehova! Ha! acuruka nanga akundisautsa ine!Akundiukira ine ndi ambiri.
2. Ambiri amati kwa moyo wanga,Alibe cipulumutso mwa Mulungu.
3. Ndipo Inu Yehova, ndinu cikopa canga;Ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.
4. Ndipfuula kwa Yehova ndi mau anga,Ndipo andiyankha m'phiri lace loyera,
5. Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo;Ndinauka; pakuti Yehova anandicirikiza.
6. Sindidzaopa unyinji wa anthu akundizinga ine.
7. Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga!Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya;Mwawatyola mano oipawo.
8. Cipulumutso nca Yehova;Dalitso lanu likhale pa anthu anu.
Werengani mutu wathunthu Masalmo 3