1. Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda m'ungwiro wanga:Ndipo ndakhulupirira Yehova, sindidzaterereka.
2. Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe;Yeretsani imso zanga ndi mtima wanga.
3. Pakuti cifundo canu ciri pamaso panga;Ndipo ndayenda m'coona canu.
4. Sindinakhala pansi ndi anthu acabe;Kapena kutsagana nao anthu otyasika.
5. Ndidana nao msonkhano wa ocimwa,Ndipo sindidzakhala nao pansi ocita zoipa.
6. Ndidzasamba manja anga mosalakwa;Kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova:
7. Kuti ndimveketse mau a ciyamiko,Ndi kulalikira nchito zanu zonse zozizwa.
8. Yehova, ndikonda cikhalidwe ca nyumba yanu,Ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.