Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 26:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda m'ungwiro wanga:Ndipo ndakhulupirira Yehova, sindidzaterereka.

2. Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe;Yeretsani imso zanga ndi mtima wanga.

3. Pakuti cifundo canu ciri pamaso panga;Ndipo ndayenda m'coona canu.

4. Sindinakhala pansi ndi anthu acabe;Kapena kutsagana nao anthu otyasika.

5. Ndidana nao msonkhano wa ocimwa,Ndipo sindidzakhala nao pansi ocita zoipa.

6. Ndidzasamba manja anga mosalakwa;Kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova:

7. Kuti ndimveketse mau a ciyamiko,Ndi kulalikira nchito zanu zonse zozizwa.

8. Yehova, ndikonda cikhalidwe ca nyumba yanu,Ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.

9. Musandicotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa,Kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi:

10. Amene m'manja mwao muli mphulupulu,Ndi dzanja lao lamanja ladzala ndi zokometsera mlandu.

11. Koma ine, ndidzayenda m'ungwiro wanga;Mundiombole, ndipo ndicitireni cifundo.

12. Phazi langa liponda pacidikha:M'masonkhano ndidzalemekeza Yehova.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 26