Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 25:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Kumbukilani, Yehova, nsoni zanu ndi cifundo canu;Pakuti izi nza kale lonse,

7. Musakumbukile zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu:Mundikumbukile monga mwa cifundo canu,Cifukwa ca ubwino wanu, Yehova.

8. Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima:Cifukwa cace adzaphunzitsa olawa za njira.

9. Adzawatsogolera ofatsa m'ciweruzo:Ndipo adzaphunzitsa ofatsa njira yace.

10. Mayendedwe onse a Yehova ndiwo cifundo ndi coonadi,Kwa iwo akusunga pangano lace ndi mboni zace.

11. Cifukwa ca dzina lanu, Yehova,Ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukuru.

12. Munthuyo wakuopa Yehova ndani?Adzamlangiza iye njira adzasankheyo.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 25