Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 25:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ceukirani ine ndipo ndicitireni cifundo;Pakuti ndiri woungumma ndi wozunzika.

17. Masautso a mtima wanga akula:Munditurutse m'zondipsinja.

18. Penyani mazunzo anga ndi zabvuta zanga;Ndipo khululukirani zolakwa zanga zonse.

19. Penyani adani anga, popeza acuruka;Ndipo andida ndi udani waciwawa.

20. Sungani moyo wanga, ndilanditseni,Ndisakhale nao manyazi, pakuti ndakhulupirira Inu.

21. Ungwiro ndi kuongoka mtima zindisunge,Pakuti ndayembekezera Inu.

22. Ombolani Israyeli, Mulungu, M'masautso ace onse.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 25