Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 25:11-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Cifukwa ca dzina lanu, Yehova,Ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukuru.

12. Munthuyo wakuopa Yehova ndani?Adzamlangiza iye njira adzasankheyo.

13. Moyo wace udzakhala mokoma;Ndi mbumba zace zidzalandira dziko lapansi.

14. Cinsinsi ca Yehova ciri kwa iwo akumuopa Iye;Ndipo adzawadziwitsa pangano lace.

15. Maso anga alinga kwa Yehova kosaleka;Pakuti Iye adzaonjola mapazi anga m'ukonde.

16. Ceukirani ine ndipo ndicitireni cifundo;Pakuti ndiri woungumma ndi wozunzika.

17. Masautso a mtima wanga akula:Munditurutse m'zondipsinja.

18. Penyani mazunzo anga ndi zabvuta zanga;Ndipo khululukirani zolakwa zanga zonse.

19. Penyani adani anga, popeza acuruka;Ndipo andida ndi udani waciwawa.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 25