Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 24:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Adzakwera ndani m'phiri la Yehova?Nadzaima m'malo ace oyera ndani?

4. Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye;Iye amene sanakweza moyo wace kutsata zacabe,Ndipo salumbira monyenga,

5. Iye adzalandira dalitso kwa Yehova,Ndi cilungamo kwa Mulungu wa cipulumutso cace.

6. Uwu ndi mbadwo wa iwo akufuna Iye,Iwo akufuna nkhope yanu, Mulungu wa Yakobo.

7. Weramutsani mitu yanu, zipata inu;Ndipo kwezekani inu, zitseko zosatha:Kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.

8. Mfumu imene ya ulemerero ndani?Yehova wamphamvu ndi wolimba,Yehova wolimba kunkhondo.

9. Weramutsani mitu yanu, zipata inu;Inde weramutsani, zitseko zosatha inu,Kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.

10. Mfumu imene ya ulemerero ndani?Yehova wa makamu makamu, Ndiye Mfumu ya ulemerero.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 24