Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 22:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?Mukhaliranji kutali kwa cipulumutso canga, ndi kwa mau a kubuula kwanga?

2. Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simubvomereza;Ndipo usiku, sindikhala cete.

3. Koma Inu ndinu woyera,Wakukhala m'malemekezo a Israyeli.

4. Makolo athu anakhulupirira Inu:Anakhulupirira, ndipo munawalanditsa.

5. Anapfuula kwa Inu, napulumutsidwa:Anakhulupita Inu, ndipo sanacita manyazi.

6. Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai:Cotonza ca anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.

7. Onse akundipenya andiseka:Akwenzula, apukusa mutu, nati,

8. Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa,Amlanditse tsopano popeza akondwera naye.

9. Pakuti Inu ndinu wondibadwitsa:Wondikhulupiritsa pokhala ine pa bere la mai wanga.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 22