1. Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu;Adzakondwera kwakukuru m'cipulumutso canu!
2. Mwampatsa iye cikhumbo ca mtimawace,Ndipo simunakana pempho la milomo yace.
3. Pakuti mumkumika iye ndi madalitso okoma:Muika korona wa golidi woyengetsa pamutu pace.
4. Anakupemphani moyo, mwampatsa iye;Mwamtalikitsira masiku ku nthawi za nthawi.
5. Ulemerero wace ngwaukuru mwa cipulumutso canu:Mumcitira iye ulemu ndi ukulu.
6. Pakuti mumuikira madalitso ku nthawi zonse;Mumkondweretsa ndi cimwemwe pankhope panu.
7. Pakuti mfumu akhulupirira Yehova,Ndipo mwa cifundo ca Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye,
8. Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse:Dzanja lanu lamanja lidzapeza iwo akuda Inu.