Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 21:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu;Adzakondwera kwakukuru m'cipulumutso canu!

2. Mwampatsa iye cikhumbo ca mtimawace,Ndipo simunakana pempho la milomo yace.

3. Pakuti mumkumika iye ndi madalitso okoma:Muika korona wa golidi woyengetsa pamutu pace.

4. Anakupemphani moyo, mwampatsa iye;Mwamtalikitsira masiku ku nthawi za nthawi.

5. Ulemerero wace ngwaukuru mwa cipulumutso canu:Mumcitira iye ulemu ndi ukulu.

6. Pakuti mumuikira madalitso ku nthawi zonse;Mumkondweretsa ndi cimwemwe pankhope panu.

7. Pakuti mfumu akhulupirira Yehova,Ndipo mwa cifundo ca Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye,

8. Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse:Dzanja lanu lamanja lidzapeza iwo akuda Inu.

9. Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu.Yehova adzawatha m'kukwiya kwace,Ndipo moto udzawanyeketsa.

10. Mudzaziononga zobala zao kuzicotsa pa dziko lapansi,Ndi mbeu zao mwa ana a anthu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 21