Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 19:3-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Palibe cilankhulidwe, palibe mau;Liu lao silimveka.

4. Muyeso wao wapitirira pa dziko lonse lapansi,Ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu.Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,

5. Ndipo liri ngati mkwati wakuturuka m'cipinda mwace,Likondwera ngati ciphona kuthamanga m'njira.

6. Kuturuka kwace lituruka kolekezera thambo,Ndipo kuzungulira kwace lifikira ku malekezero ace:Ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwace.

7. Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo;Mboni za Yehova ziri zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru;

8. Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima:Malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.

9. Kuopa Yehova kuli mbe, kwakukhalabe nthawi zonse:Maweruzo a Yehova ali oona, alungama konse konse.

10. Ndizo zifunika koposa golidi, inde, golidi wambiri woyengetsa:Zizuna koposa uci ndi zakukha za zisa zace,

11. Ndiponso kapolo wanu acenjezedwa nazo:M'kuzisunga izo muli mphotho yaikuru.

12. Adziwitsa zolowereza zace ndani?Mundimasule kwa zolakwa zobisika.

13. Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama;Zisacite ufumu pa ine: pamenepo ndidzakhala wangwiro,Ndi wosacimwa colakwa cacikuru.

14. Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga abvomerezeke pamaso panu,Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 19