40. Ndipo adani anga mwawalozetsa m'mbuyo kwa ine,Kuti ndipasule ondidawo.
41. Anapfuula, koma panalibewopulumutsa;Ngakhale kwa Yehova, koma sanawabvomereza.
42. Pamenepo ndinawapera ngati pfumbi la kumphepo;Ndinawakhuthula ngati matope a pabwalo.
43. Mwandipulumutsa pa zolimbana nane za anthu;Mwandiika mutu wa amitundu;Mtundu wa anthu sindinaudziwa udzanditumikira.
44. Pakumva m'khutu za ine adzandimvera:Alendo adzandigonjera monyenga.
45. Alendo adzafota,Nadzaturuka monjenjemera m'ngaka mwao.
46. Yehova ngwa moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;Nakwezeke Mulungu wa cipulumutso canga: