Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 18:28-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Pakuti Inu muyatsa nyali yanga;Yehova, Mulungu wanga, aunikira mdima wanga.

29. Pakuti mwa Inu ndipyola khamu la anthu;Ndipo mwa Mulungu wanga ndilumphira linga.

30. Mulungu ndiyewangwiro m'njira zace;Mau a Yehova ngoyengeka; Ndiye cikopa ca onse okhulupirira Iye.

31. Pakuti Mulungu ndani wosati Yehova?Ndipo thanthwe ndani wosati Mulungu wathu?

32. Mulungu ndiye wondizingiza mphamvu m'cuuno,Nakonza njira yanga ikhale yangwiro.

33. Alinganiza mapazi anga ngati a nswala:Nandiimitsa pamsanje panga.

34. Aphunzitsa manja anga agwire nkhondo;Kuti walifuka uta wamkuwa ndi manja anga.

35. Ndipo mwandipatsa cikopa ca cipulumutso canu:Ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza,Ndipo cifatso canu candikuza ine.

36. Mwandipondetsa patali patali,Sanaterereka mapazi anga.

37. Ndidzalondola adani anga, ndi kuwapeza:Ndipo sindidzabwerera asanathe psiti.

38. Ndidzawapyoza kuti sangakhoze kuuka:Adzagwa pansi pa mapazi anga,

39. Pakuti mwaudizingiza mphamvu m'cuuno ku nkhondoyo:Mwandigonjetsera amene andiukira.

40. Ndipo adani anga mwawalozetsa m'mbuyo kwa ine,Kuti ndipasule ondidawo.

41. Anapfuula, koma panalibewopulumutsa;Ngakhale kwa Yehova, koma sanawabvomereza.

42. Pamenepo ndinawapera ngati pfumbi la kumphepo;Ndinawakhuthula ngati matope a pabwalo.

43. Mwandipulumutsa pa zolimbana nane za anthu;Mwandiika mutu wa amitundu;Mtundu wa anthu sindinaudziwa udzanditumikira.

44. Pakumva m'khutu za ine adzandimvera:Alendo adzandigonjera monyenga.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 18