Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 18:18-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Anandipeza ine tsiku la tsoka langa;Koma Yehova anali mcirikizo wanga.

19. Ananditurutsanso andifikitse motakasuka;Anandilanditsa, pakuti anakondwera ndi ine.

20. Yehova anandibwezera monga mwa cilungamo canga;Anandisudzula monga mwa kusisira kwa manja anga.

21. Pakuti ndasunga njira za Yehova,Ndipo sindinacitira coipa kusiyana ndi Mulungu wanga.

22. Pakuti maweruzo ace onse anali pamaso panga,Ndipo malemba ace sindinawacotsa kwa ine.

23. Ndipo ndinakhala wangwiro ndi iye,Ndipo ndinadzisunga wosacita coipa canga.

24. Ndimo anandisudzulira Yehova monga mwa cilungamo canga,Monga mwa kusisira kwa manja anga pamaso pace.

25. Pa wacifundo mukhala wacifundoPa mumthu wangwiro mukhala wangwiro;

26. Pa woyera mtima mukhala woyera mtima;Pa wotsutsatsutsa mukhala wotsutsana naye.

27. Pakuti Inu muwapulumutsa anthu aumphawi;Koma maso okweza muwatsitsa.

28. Pakuti Inu muyatsa nyali yanga;Yehova, Mulungu wanga, aunikira mdima wanga.

29. Pakuti mwa Inu ndipyola khamu la anthu;Ndipo mwa Mulungu wanga ndilumphira linga.

30. Mulungu ndiyewangwiro m'njira zace;Mau a Yehova ngoyengeka; Ndiye cikopa ca onse okhulupirira Iye.

31. Pakuti Mulungu ndani wosati Yehova?Ndipo thanthwe ndani wosati Mulungu wathu?

Werengani mutu wathunthu Masalmo 18