Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 18:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndikukondani, Yehova, mphamvu yanga.

2. Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi mpulumutsi wanga;Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye;Cikopa canga, nyanga ya cipulumutso canga, msanje wanga.

3. Ndidzaitanira Yehova, woyenera kutamandika:Ndipo adzandipulumutsa ine kwa adani anga.

4. Zingwe za imfa zinandizinga,Ndipo mitsinje ya zopanda pace inandiopsa.

5. Zingwe za manda zinandizinga:Misampha ya imfa inandifikira ine.

6. M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova,Ndipo ndinakuwira Mulungu wanga;Mau anga anawamva m'Kacisi mwace,Ndipo mkuwo wanga wa pankhope pace unalowa m'makutu mwace.

7. Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi.Ndi maziko a mapiri ananjenjemeraNagwedezeka, pakuti anakwiya iyeyo.

8. Unakwera utsi woturuka m'mphuno mwace:Ndi moto wa m'kamwa mwace unanyeka:Nuyakitsa makara.

9. Ndipo Iye anaweramitsa thambo, natsika;Ndipo pansi pa mapazi ace panali mdima bii.

10. Ndipo anaberekeka pa kerubi, nauluka;Nauluka msanga pa mapiko a mphepo,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 18