1. Haleluya,Lemekezani Mulungu m'malo ace oyera;Mlemekezeni m'thambo la mphamvu yace.
2. Mlemekezeni cifukwa ca nchito zace zolimba;Mlemekezeni monga mwa ukulu wace waunjinji.
3. Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga;Mlemekezeni ndi cisakasa ndi zeze.
4. Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe:Mlemekezeni ndi zoyimbira za zingwe ndi citoliro.
5. Mlemekezeni ndi nsanje zomveka:Mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa.