Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 146:7-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndiye wakucitira ciweruzo osautsika;Ndiye wakupatsa anjala cakudya;Yehova amasula akaidi;

8. Yehova apenyetsa osaona;Yehova aongoletsa onse owerama;Yehova akonda olungama;

9. Yehova asunga alendo;Agwiriziza mwana wamasiye mkazi wamasiye;Koma akhotetsa njira ya oipa.

10. Yehova adzacita ufumu kosatha,Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwo mibadwo.Haleluya.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 146