Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 145:6-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo adzanenera mphamvu za nchito zanu zoopsa;Ndi ukulu wanu ndidzaufotokozera.

7. Adzabukitsa cikumbukilo ca ubwino wanu waukuru,Nadzayimbira cilungamo canu.

8. Yehova ndiye wacisomo, ndi wacifundo;Osakwiya msanga, ndi wa cifundo cacikuru.

9. Yehova acitira cokoma onse;Ndi nsoni zokoma zace zigwera nchito zace zonse.

10. Nchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova;Ndi okondedwa anu adzakulemekezani.

11. Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu,Adzalankhulira mphamvu yanu;

12. Kudziwitsa ana a anthu zamphamvu zace,Ndi ulemerero waukuru wa ufumu wace.

13. Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya,Ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonse yonse.

14. Yehova agwiriziza onse akugwa,Naongoletsa onse owerama.

15. Maso a onse ayembekeza Inu;Ndipo muwapatsa cakudya cao m'nyengo zao.

16. Muniowetsa dzanja lanu,Nimukwaniritsira zamoyo zonse cokhumba cao.

17. Yehova ali wolungama m'njira zace zonse,Ndi wacifundo m'nchito zace zonse.

18. Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye,Onse akuitanira kwa Iye m'coonadi.

19. Adzacita cokhumba iwo akumuopa;Nadzamva kupfuula kwao, nadzawapulumutsa.

20. Yehova asunga onse akukondana naye;Koma oipa onse adzawaononga.

21. Pakamwa panga padzanena cilemekezo ca Yehova;Ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lace loyera ku nthawi za nthawi.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 145