4. Mbadwo wina udzalemekezera nchito zanu mbadwo unzace,Ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.
5. Ndidzalingalira ulemerero waukuru wa ulemu wanu,Ndi nchito zanu zodabwiza.
6. Ndipo adzanenera mphamvu za nchito zanu zoopsa;Ndi ukulu wanu ndidzaufotokozera.
7. Adzabukitsa cikumbukilo ca ubwino wanu waukuru,Nadzayimbira cilungamo canu.
8. Yehova ndiye wacisomo, ndi wacifundo;Osakwiya msanga, ndi wa cifundo cacikuru.
9. Yehova acitira cokoma onse;Ndi nsoni zokoma zace zigwera nchito zace zonse.
10. Nchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova;Ndi okondedwa anu adzakulemekezani.
11. Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu,Adzalankhulira mphamvu yanu;
12. Kudziwitsa ana a anthu zamphamvu zace,Ndi ulemerero waukuru wa ufumu wace.
13. Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya,Ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonse yonse.
14. Yehova agwiriziza onse akugwa,Naongoletsa onse owerama.
15. Maso a onse ayembekeza Inu;Ndipo muwapatsa cakudya cao m'nyengo zao.
16. Muniowetsa dzanja lanu,Nimukwaniritsira zamoyo zonse cokhumba cao.
17. Yehova ali wolungama m'njira zace zonse,Ndi wacifundo m'nchito zace zonse.