Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 145:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu;Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.

2. Masiku onse ndidzakuyamikani;Ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.

3. Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukuru;Ndi ukulu wace ngwosasanthulika.

4. Mbadwo wina udzalemekezera nchito zanu mbadwo unzace,Ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.

5. Ndidzalingalira ulemerero waukuru wa ulemu wanu,Ndi nchito zanu zodabwiza.

6. Ndipo adzanenera mphamvu za nchito zanu zoopsa;Ndi ukulu wanu ndidzaufotokozera.

7. Adzabukitsa cikumbukilo ca ubwino wanu waukuru,Nadzayimbira cilungamo canu.

8. Yehova ndiye wacisomo, ndi wacifundo;Osakwiya msanga, ndi wa cifundo cacikuru.

9. Yehova acitira cokoma onse;Ndi nsoni zokoma zace zigwera nchito zace zonse.

10. Nchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova;Ndi okondedwa anu adzakulemekezani.

11. Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu,Adzalankhulira mphamvu yanu;

Werengani mutu wathunthu Masalmo 145