Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 141:7-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Mafupa athu amwazika pakamwa pa manda,Monga ngati akumba nanyimphula nthaka yapansi.

8. Pakuti maso anga apenya kwanu, Yehova Ambuye;Ndithawira kwa Inu; musataye moyowanga.

9. Mundisunge ndisagwe mumsampha anandicherawo,Ndisakodwe m'makwekwe a iwo ocita zopanda pace,

10. Oipa agwe pamodzi m'maukonde ao,Kufikira nditapitirira ine.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 141