Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 141:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine;Mundicherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu.

2. Pempherolanga liikike ngaticofukiza pamaso panu;Kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.

3. Muike mdindo pakamwa panga, Yehova;Sungani pakhomo pa milomo yanga.

4. Mtima wanga usalinge ku cinthu coipa,Kucita nchito zoipaNdi anthu akucita zopanda pace;Ndipo ndisadye zankhuli zao.

5. Akandipanda munthu wolungama ndidzati ncifundo:Akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu;Mutu wanga usakane:Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.

6. Oweruza ao anagwetseka pambali pa thanthwe;Nadzamva mau anga kuti ndiwo okondweretsa.

7. Mafupa athu amwazika pakamwa pa manda,Monga ngati akumba nanyimphula nthaka yapansi.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 141