Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 14:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Waucitsiru amati mumtima mwace, Kulibe Mulungu.Acita zobvunda, acita nchito zonyansa;Kulibe wakucita bwino.

2. Yehova m'Mwamba anaweramira pa ana a anthu,Kuti aone ngati aliko wanzeru,Wakufuna Mulungu.

3. Anapatuka onse; pamodzi anabvunda mtima;Palibe wakucita bwino ndi mmodzi yense.

4. Kodi onse ocita zopanda pace sadziwa kanthu?Pakudya anthu anga monga akudya mkate,Ndipo saitana pa Yehova.

5. Pamenepa anaopa-opatu:Pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama.

6. Munyazitsa uphungu wa wozunzika,Koma Yehova ndiye pothawira pace.

7. Mwenzi cipulumutso ca Israyeli citacokera ku Ziyoni!Pakubweretsa Yehova anthu ace a m'nsinga,Pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 14