Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 138:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Tsiku loitana ine, munandiyankha,Munandilimbitsa ndi mphamvu m'moyo mwanga.

4. Mafumu onse a pa dziko lapansi adzakuyamikani,Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu.

5. Ndipo adzayimbira njira za Yehova;Pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukuru.

6. Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo;Koma wodzikuza amdziwira kutali.

7. Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo;Mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu,Ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.

8. Yehova adzanditsirizira za kwa ine:Cifundo canu, Yehova, cifikira ku nthawi zonse:Musasiye nchito za manja anu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 138