Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 138:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndidzakuyamikani ndi mtima wangawonse;Ndidzayimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu,

2. Ndidzagwadira kuloza ku Kacisi wanu woyera,Ndi kuyamika dzina lanu,Cifukwa ca cifundo canu ndi coonadi canu;Popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.

3. Tsiku loitana ine, munandiyankha,Munandilimbitsa ndi mphamvu m'moyo mwanga.

4. Mafumu onse a pa dziko lapansi adzakuyamikani,Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 138