Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 135:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Sihoni mfumu ya Aamori,Ndi Ogi mfumu ya Basana,Ndi maufumu onse a Kanani:

12. Ndipo anapereka dziko lao likhale cosiyira,Cosiyira ca kwa Israyeli anthu ace.

13. Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha;Cikumbukilo canu, Yehova, kufikira mibadwo mibadwo.

14. Pakuti Yehova adzaweruza anthu ace,Koma adzaleka atumiki ace.

15. Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golidi,Nchito ya manja a anthu.

16. Pakamwa ali napo koma osalankhula;Maso ali nao, koma osapenya;

17. Makutu ali nao, koma osamva;Inde, pakamwa pao palibe mpweya.

18. Akuwapanga adzafanana nao;Inde, onse akuwakhulupirira.

19. A nyumba ya Israyeli inu, lemekezani Yehova:A nyumba ya Aroni inu, lemekezani Yehova:

20. A nyumba ya Levi inu, lemekezani Yehova:Inu akuopa Yehova, lemekezani Yehova.

21. Alemekezedwe Yehova kucokera m'Ziyoni,Amene akhala m'Yerusalemu.Haleluya,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 135