Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 133:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithuKuti abale akhale pamodzi!

2. Ndiko ngati mafuta a mtengo wace pamutu,Akutsikira ku ndebvu,Inde ku ndebvu za Aroni;Akutsikira ku mkawo wa zobvala zace

3. Ngati mame a ku Hermoni,Akutsikira pa mapiri a Ziyoni:Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo,Ndilo moyo womka muyaya,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 133