Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 130:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. M'mozamamo ndinakupfuulirani, Yehova.

2. Ambuye, imvani liu langa;Makutu anu akhale cimverereMau a kupemba kwanga.

3. Mukasunga mphulupulu, Yehova,Adzakhala ciriri ndani, Ambuye?

4. Koma kwa Inu kuli cikhululukiro,Kuti akuopeni.

5. Ndilindira Yehova, moyo wanga ulindira,Ndiyembekeza mau ace.

6. Moyo wanga uyang'anira Ambuye,Koposa alonda matanda kuca;Inde koposa alonda matanda kuca.

7. Israyeli, uyembekezere Yehova;Cifukwa kwa Yehova kuli cifundo,Kwaonso kucurukira ciombolo.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 130