Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 127:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Akapanda kumanga nyumba Yehova,Akuimanga agwiritsa nchito cabe;Akapanda kusunga mudzi Yehoya,Mlonda adikira cabe.

2. Kuli cabe kwa inu Rulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo,Kudya mkate wosautsa kuupeza;Kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ace ngati m'tulo.

3. Taonani ana ndiwo colandira ca kwa Yehova;Cipatso ca m'mimba ndico mphotho yace.

4. Ana a ubwana wace wa munthuAkunga mibvi m'dzanja lace la ciphona.

5. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lace:Sadzacita manyazi iwo,Pakulankhula nao adani kucipata.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 127