Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 125:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Iwo akukhulupirira YehovaAkunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha,

2. Monga mapiri azinga Yerusalemu,Momwemo Yehova azinga anthu ace,Kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

3. Pakuti ndodo yacifumu ya coipa siidzapumula pa gawo la olungama;Kuti olungama asaturutse dzanja lao kucita cosalungama,

4. Citirani cokoma, Yehova, iwo okhala okoma;Iwo okhala oongoka mumtima mwao.

5. Koma iwo akupatuka kutsata njira zao zokhotakhota,Yehova adzawacotsa pamodzi ndi ocita zopanda pace.Mtendere ukhale pa Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 125