Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 124:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Akadapanda kukhala nafe Yehova,Anene tsono Israyeli;

2. Akadapanda kukhala nafe Yehova,Pakutiukira anthu:

3. Akadatimeza amoyo,Potipsera mtima wao.

4. Akadatimiza madziwo,Mtsinje ukadapita pa moyo wathu;

5. Madzi odzikuza akadapita pa moyo wathu.

6. Alemekezedwe Yehova,Amene sanatipereka kumano kwao tikhale cakudya cao.

7. Moyo wathu unaonjoka ngati mbalame mu msampha wa msodzi;Msampha unatyoka ndi ife tinaonioka.

8. Thandizo lathu liri m'dzina la Yehova,Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 124