Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 122:4-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova;Akhale mboni ya kwa Israyeli,Ayamike dzina la Yehova.

5. Pakuti pamenepo anaika mipando ya ciweruzo,Mipando ya nyumba ya Davide.

6. Mupempherere mtendere wa Yerusalemu;Akukonda inu adzaona phindu.

7. M'linga mwako mukhale mtendere,M'nyumba za mafumu mukhale phindu.

8. Cifukwa ca abale anga ndi mabwenzi anga,Ndidzanena tsopano, Mukhale mtendere mwa inu.

9. Cifukwa ca nyumba ya Yehova Mulungu wathuNdidzakufunira zokoma,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 122