Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 122:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndinakondwera m'mene ananena nane,Tiyeni ku nyumba ya Yehova.

2. Mapazi athu alinkuima M'zipata zanu, Yerusalemu.

3. Yerusalemu anamangidwaNgati mudzi woundana bwino:

4. Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova;Akhale mboni ya kwa Israyeli,Ayamike dzina la Yehova.

5. Pakuti pamenepo anaika mipando ya ciweruzo,Mipando ya nyumba ya Davide.

6. Mupempherere mtendere wa Yerusalemu;Akukonda inu adzaona phindu.

7. M'linga mwako mukhale mtendere,M'nyumba za mafumu mukhale phindu.

8. Cifukwa ca abale anga ndi mabwenzi anga,Ndidzanena tsopano, Mukhale mtendere mwa inu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 122