Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 12:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa;Pakuti okhulupirika acepa mwa ana a anthu.

2. Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wace:Amanena ndi mlomo wotyasika, ndi mitima iwiri.

3. Yehova adzadula milomo yonse yotyasika,Lilime lakudzitamandira:

4. Amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa;Milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?

5. Cifukwa ca kupasuka kwa ozunzika, cifukwa ca kuusa moyo kwa aumphawi,Ndiuka tsopano, ati Yehova; Ndidzamlonga mosungika muja alaka-lakamo.

6. Mau a Yehova ndi mau oona;Ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi,Yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.

7. Mudzawasunga, Yehova,Mudzawacinjirizira mbadwo uno ku nthawi zonse.

8. Oipa amayenda mozungulira-zungulira,Potamanda iwo conyansa mwa ana a anthu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 12