Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 119:75-90 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

75. Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova,Ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika.

76. Cifundo canu cikhaletu cakunditonthoza, ndikupemphani,Monga mwa mau anu kwa mtumiki wanu.

77. Nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo;Popeza cilamulo canu cindikondweretsa.

78. Odzikuza acite manyazi, popeza anandicitira monyenga ndi bodza:Koma ine ndidzalingalira malangizo anu.

79. Iwo akuopa Inu abwere kwa ine,Ndipo adzadziwa mboni zanu.

80. Mtima wanga ukhale wangwiro m'malemba anu;Kuti ndisacite manyazi.

81. Moyo wanga unakomoka ndi kukhumba cipulumutso canu:Ndinayembekezera mau anu.

82. Maso anga anatha mphamvu ndi kukhumba mau anu,Ndikuti, Mudzanditonthoza liti?

83. Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira;Koma sindiiwala malemba anu.

84. Masiku a mtumiki wanu ndiwo angati?Mudzaweruza liti iwo akundilondola koipa?

85. Odzikuza anandikumbira mbuna,Ndiwo osasamalira cilamulo canu.

86. Malamulo anu onse ngokhulupirika;Andilondola nalo bodza; ndithandizeni.

87. Akadandithera pa dziko lapansi; Koma ine sindinasiya malangizo anu.

88. Mundipatse moyo monga mwa cifundo canu;Ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu,

89. Mau anu aikika kumwamba,Kosatha, Yehova.

90. Cikhulupiriko canu cifikira mibadwo mibadwo;Munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 119