39. Mundipatutsire cotonza canga ndiciopaco;Popeza maweruzo anu ndi okoma.
40. Taonani, ndinalira malangizo anu;Mundipatse moyo mwa cilungamo canu.
41. Ndipo cifundo canu cindidzere, Yehova,Ndi cipulumutso canu, monga mwa mau anu.
42. Kuti ndikhale nao mau akuyankha wonditonza;Popeza ndikhulupirira mau anu.
43. Ndipo musandicotsere ndithu mau a coonadi pakamwa panga;Pakuti ndinayembekeza maweruzo anu.
44. Potero ndidzasamalira malamulo anu cisamalireKu nthawi za nthawi.
45. Ndipo ndidzayenda mwaufulu;Popeza ndinafuna malangizo anu.
46. Ndidzalankhulanso za umboni wanu pamaso pa mafumu,Osacitapo manyazi.
47. Ndipo ndidzadzikondweretsa nao malamulo anu,Amene ndiwakonda.
48. Ndidzakwezanso manja anga ku malamulo anu, amene ndiwakonda;Ndipo ndidzalingalira pa malemba anu.
49. Kumbukilani mau a kwa mtumiki wanu,Amene munandiyembekezetsa nao.
50. Citonthozo canga m'kuzunzika kwanga ndi ici;Pakuti mau anu anandipatsa moyo.
51. Odzikuza anandinyoza kwambiri:Koma sindinapatukanso naco cilamulo canu.
52. Ndinakumbukila maweruzo anu kuyambira kale, Yehova,Ndipo ndinadzitonthoza.
53. Ndinasumwa kwakukuru,Cifukwa ca oipa akusiya cilamulo canu.