Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 119:31-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Ndimamatika nazo mboni zanu;Musandicititse manyazi, Yehova.

32. Ndidzathamangira njira ya malamulo anu,Mutakulitsa mtima wanga.

33. Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu;Ndidzaisunga kufikira kutha kwace.

34. Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu;Ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.

35. Mundiyendetse mopita malamulo anu;Pakuti ndikondwera m'menemo.

36. Lingitsani mtima wanga ku mboni zanu,Si ku cisiriro ai.

37. Mucititse mlubza maso anga ndisapenye zacabe,Mundipatse moyo mu njira yanu.

38. Limbitsirani mtumiki wanu mau anu,Ndiye wodzipereka kukuopani.

39. Mundipatutsire cotonza canga ndiciopaco;Popeza maweruzo anu ndi okoma.

40. Taonani, ndinalira malangizo anu;Mundipatse moyo mwa cilungamo canu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 119