163. Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo;Koma ndikonda cilamulo canu.
164. Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi,Cifukwa ca maweruzo anu alungama.
165. Akukonda cilamulo canu ali nao mtendere wambiri;Ndipo alibe cokhumudwitsa.
166. Ndinayembekeza cipulumutso canu, Yehova,Ndipo ndinacita malamulo anu.
167. Moyo wanga unasamalira mboni zanu;Ndipo ndizikonda kwambiri.
168. Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu;Popeza njira zanga zonse ziri pamaso panu,
169. Kupfuula kwanga kuyandikire pamaso pano, Yehova;Mundizindikiritse monga mwa mau anu.
170. Kupemba kwanga kudze pamaso panu;Mundilanditse monga mwa mau anu.
171. Milomo yanga iturutse cilemekezo;Popeza mundiphunzitsa malemba anu.
172. Lilime langa liyimbire mau anu;Pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama.
173. Dzanja lanu likhale lakundithandizaPopezandinasankha malangizo anu.
174. Ndinakhumba cipulumutso canu, Yehova;Ndipo cilamulo canu ndico condikondweretsa.
175. Mzimu wanga ukhale ndi moyo, ndipo udzakulemekezani;Ndipo maweruzo anu andithandize.
176. Ndinasocera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu;Pakuti sindiiwala malamulo anu.