158. Ndinapenya ocita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao;Popeza sasamalira mau anu.
159. Penyani kuti ndikonda malangizo anu;Mundipatse moyo, Yehova, monga mwa cifundo canu.
160. Ciwerengero ca mau anu ndico coonadi;Ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.
161. Nduna zinandilondola kopanda cifukwa;Koma mtima wanga ucita mantha nao mau anu.
162. Ndikondwera nao mau anu,Ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri.
163. Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo;Koma ndikonda cilamulo canu.
164. Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi,Cifukwa ca maweruzo anu alungama.
165. Akukonda cilamulo canu ali nao mtendere wambiri;Ndipo alibe cokhumudwitsa.
166. Ndinayembekeza cipulumutso canu, Yehova,Ndipo ndinacita malamulo anu.
167. Moyo wanga unasamalira mboni zanu;Ndipo ndizikonda kwambiri.