Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 119:143-146 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

143. Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera;Koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.

144. Mboni zanu ndizo zolungama kosatha;Mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo.

145. Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova;Ndidzasunga malemba anu.

146. Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni,Ndipo ndidzasamalira mboni zanu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 119