Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 119:139-151 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

139. Cangu canga cinandithera,Popeza akundisautsa anaiwala mau anu.

140. Mau anu ngoyera ndithu;Ndi mtumiki wanu awakonda.

141. Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa;Koma sindiiwala malemba anu.

142. Cilungamo canu ndico cilungamo cosatha;Ndi cilamulo canu ndico coonadi.

143. Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera;Koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.

144. Mboni zanu ndizo zolungama kosatha;Mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo.

145. Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova;Ndidzasunga malemba anu.

146. Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni,Ndipo ndidzasamalira mboni zanu.

147. Ndinapfuula kusanace:Ndinayembekezera mau anu.

148. Maso anga anakumika malonda a usiku,Kuti ndilingirire mau anu.

149. Imvani liu langa monga mwa cifundo canu;Mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova.

150. Otsata zaciwembu andiyandikira;Akhala kutali ndi cilamulo canu.

151. Inu muli pafupi, Yehova;Ndipo malamulo anu onse ndiwo coonadi,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 119