Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 119:120-139 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

120. Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu;Ndipo ndicita mantha nao maweruzo anu.

121. Ndinacita ciweruzo ndi cilungamo;Musandisiyira akundisautsa.

122. Mumkhalire cikole mtumiki wanucimkomere;Odzikuza asandisautse.

123. Maso anga anatha mphamvu pafuna cipulumutso canu,Ndi mau a cilungamo canu.

124. Mucitire mtumiki wanu monga mwa cifundo canu,Ndipo ndiphunzitseni malemba anu,

125. Ine ndine mtumiki wanu, ndizindikiritseni;Kuti ndidziwe mboni zanu.

126. Yafika nyengo yakuti Yehova acite kanthu;Pakuti anaswa cilamulo canu.

127. Cifukwa cace ndikonda malamulo anuKoposa golidi, Inde golidi woyengeka,

128. Cifukwa cace ndiyesa ngolunjika malangizo anu onse akunena zonse;Koma ndidana nazo njira zonse zonyenga.

129. Mboni zanu nzodabwiza; Cifukwa cace moyo wanga uzisunga,

130. Potsegulira mau anu paunikira;Kuzindikiritsa opusa.

131. Ndinatsegula pakamwa panga, ndi kupuma wefu wefu;Popeza ndinakhumba malamulo anu.

132. Munditembenukire, ndi kundicitira cifundo,Monga mumatero nao akukonda dzina lanu.

133. Kfiazikitsanimapaziangam'mau anu;Ndipo zisandigonjetse zopanda pace ziri zonse.

134. Mundiombole ku nsautso ya munthu:Ndipo ndidzasamalira malangizo anu.

135. Muwalitse nkhope yanu pa mtumiki wanu;Ndipo mundiphunzitse malemba anu.

136. Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi,Popeza sasamalira cilamulo canu.

137. Inu ndinu wolungama, Yehova,Ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika.

138. Mboni zanuzo mudazilamuliraZiri zolungama ndi zokhulupirika ndithu.

139. Cangu canga cinandithera,Popeza akundisautsa anaiwala mau anu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 119