115. Mundicokere ocita zoipa inu;Kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.
116. Mundicirikize monga mwa mau anu, kuti ndikhale ndi moyo;Ndipo ndisacite manyazi pa ciyembekezo canga.
117. Mundigwirizize ndipo ndidzapulumutsidwa,Ndipo ndidzasamalira malemba anu cisamalire.
118. Mupepulaonseakusokeram'malemba anu;Popeza cinyengo cao ndi bodza.
119. Mucotsa oipa onse a pa dziko lapansi ngati mphala:Cifukwa cace ndikonda mboni zanu.
120. Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu;Ndipo ndicita mantha nao maweruzo anu.
121. Ndinacita ciweruzo ndi cilungamo;Musandisiyira akundisautsa.
122. Mumkhalire cikole mtumiki wanucimkomere;Odzikuza asandisautse.
123. Maso anga anatha mphamvu pafuna cipulumutso canu,Ndi mau a cilungamo canu.
124. Mucitire mtumiki wanu monga mwa cifundo canu,Ndipo ndiphunzitseni malemba anu,