Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 119:104-113 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

104. Malangizo anu andizindikiritsa;Cifukwa cace ndidana nao mayendedwe onse acinyengo,

105. Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga,Ndi kuunika kwa panjira panga,

106. Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima,Kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.

107. Ndazunzika kwambiri:Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu.

108. Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga,Ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu.

109. Moyo wanga ukhala m'dzanja langa cikhalire;Koma sindiiwala cilamulo canu.

110. Oipa anandichera msampha;Koma sindinasokera m'malangizo anu.

111. Ndinalandira mboni zanu zikhale colandira cosatha;Pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.

112. Ndinalingitsa mtima wanga ucite malemba anu,Kosatha, kufikira cimatiziro.

113. Ndidana nao a mitima iwiri;Koma ndikonda cilamulo canu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 119