Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 119:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Odala angwiro m'mayendedwe ao,Akuyenda m'cilamulo ca Yehova.

2. Odala iwo akusunga mboni zace,Akumfuna ndi mtima wonse;

3. Inde, sacita cosalungama;Ayenda m'njira zace.

4. Inu munatilamulira.Tisamalire malangizo anu ndi cangu,

5. Ha! mwenzi zitakhazikika njira zangaKuti ndisamalire malemba anu.

6. Pamenepo sindidzacita manyazi,Pakupenyerera malamulo anu onse.

7. Ndidzakuyanrikani ndi mtima woongoka,Pakuphunzira maweruzo anu olungama.

8. Ndidzasamalira malemba anu:Musandisiye ndithu.

9. Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ace bwanji?Akawasamalira monga mwa mau anu.

10. Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse;Ndisasokere kusiyana nao malamulo anu.

11. Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga,Kuti ndisalakwire Inu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 119