1. Ndimkonda, popeza Yehova amamva,Mau anga ndi kupemba kwanga.
2. Popeza amandicherera khutu lace,Cifukwa cace ndidzaitanira Iye masiku anga onse.
3. Zingwe za imfa zinandizinga,Ndi zowawa za manda zinandigwira:Ndinapeza nsautso ndi cisoni.
4. Pamenepo ndinaitana dzina la Yehova;Ndikuti, Yehova ndikupemphani landitsani moyo wanga.
5. Yehova ngwa cifundo ndi wolungama;Ndi Mulungu wathu ngwa nsoni.
6. Yehova asunga opusa;Ndidafoka ine, koma anandipulumutsa,
7. Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako;Pakuti Yehova anakucitira cokoma.
8. Pakuti munalanditsa moyo wanga kuimfa,Maso anga kumisozi, Mapazi anga, ndingagwe.
9. Ndidzayenda pamaso pa Yehova M'dziko la amoyo.
10. Ndinakhulupirira, cifukwa cace ndinalankhula;Ndinazunzika kwambiri.