Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 115:5-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pakamwa ali napo, koma osalankhula;Maso ali nao, koma osapenya;

6. Makutu ali nao, koma osamva;Mphuno ali nazo, koma osanunkhiza;

7. Manja ali nao, koma osagwira;Mapazi ali nao, koma osayenda;Kapena sanena pammero pao,

8. Adzafanana nao iwo akuwapanga;Ndi onse akuwakhulupirira,

9. Israyeli, khulupirira Yehova:Ndiye mthandizi wao ndi cikopa cao.

10. Nyumba ya Aroni, khulupirira Yehova:Ndiye mthandizi wao, ndi cikopa cao.

11. Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova;Ndiye mthandizi wao ndi cikopa cao.

12. Yehova watikumbukila; adzatidalitsa:Adzadalitsa nyumba ya Israyeli;Adzadalitsa nyumba ya Aroni.

13. Adzadalitsa iwo akuopa Yehova,Ang'ono ndi akuru.

14. Yehova akuonjezereni dalitso, Inu ndi ana anu.

15. Odalitsika inu a kwa Yehova,Wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.

16. Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova;Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.

17. Akufa salemekeza Yehova,Kapena ali yense wakutsikira kuli cete:

18. Koma ife tidzalemekeza YehovaKuyambira tsopano kufikira nthawi yonse.Haleluya.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 115