Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 115:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, Koma kwa dzina lanu patsani ulemerero,Cifukwa ca cifundo canu, ndi coonadi canu.

2. Aneneranji amitundu,Ali kuti Mulungu wao?

3. Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba;Acita ciri conse cimkonda.

4. Mafano ao ndiwo a siliva ndi golidi,Nchito za manja a anthu.

5. Pakamwa ali napo, koma osalankhula;Maso ali nao, koma osapenya;

6. Makutu ali nao, koma osamva;Mphuno ali nazo, koma osanunkhiza;

7. Manja ali nao, koma osagwira;Mapazi ali nao, koma osayenda;Kapena sanena pammero pao,

8. Adzafanana nao iwo akuwapanga;Ndi onse akuwakhulupirira,

9. Israyeli, khulupirira Yehova:Ndiye mthandizi wao ndi cikopa cao.

10. Nyumba ya Aroni, khulupirira Yehova:Ndiye mthandizi wao, ndi cikopa cao.

11. Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova;Ndiye mthandizi wao ndi cikopa cao.

12. Yehova watikumbukila; adzatidalitsa:Adzadalitsa nyumba ya Israyeli;Adzadalitsa nyumba ya Aroni.

13. Adzadalitsa iwo akuopa Yehova,Ang'ono ndi akuru.

14. Yehova akuonjezereni dalitso, Inu ndi ana anu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 115