Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 114:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. M'mene Israyeli anaturuka ku Aigupto,Nyumba ya Yakobo kwa anthu a cinenedwe cacilendo;

2. Yuda anakhala malo ace oyera, Israyeli ufumu wace.

3. Nyanjayo inaona, nithawa;Yordano anabwerera m'mbuyo.

4. Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo,Timapiri ngati ana a nkhosa.

5. Unathawanji nawe, nyanja iwe?Unabwerereranji m'mbuyo, Yordano iwe?

6. Munatumpha-tumphiranji ngati nkhosa zamphongo, mapiri inu?Ngati ana a nkhosa, zitunda inu?

7. Unjenjemere, dziko lapansi iwe, pamaso pa Ambuye,Pamaso pa Mulungu wa Yakobo;

8. Amene anasanduliza thanthwe likhale thawale lamadzi,Nsangalabwi ikhale kasupe wamadzi.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 114